1 Kings 11:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanyamuka ku Midiyani, napita ku Parani, ndipo adatengako amuna ena ku Paraniko, nakafika ku Ejipito kwa mfumu Farao. Farao adapatsa Hadadi ndi anthu ake nyumba ndi chakudya, namninkhanso kadziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacoka ku Midyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Aigupto kwa Farao mfumu ya Aigupto, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.