1 Kings 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akazi ameneŵa anali a mitundu ija imene Chauta adaauza Aisraele kuti, “Musadzakwatire akazi a mitundu imeneyi, ndipo amuna amitunduyo asadzakwatire akazi a mtundu wanu, poti ndithudi iwowo adzatembenuza mitima yanu, kuti muzitsata milungu yao.” Koma Solomoni ankakondabe akazi a mitundu imeneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israyeli za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomo anawaumirira kuwakonda.