1 Kings 11:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Hadadi atamva ku Ejipitoko kuti Davide adamwalira, ndiponso kuti Yowabu mtsogoleri wankhondo nayenso adafa, adauza Farao kuti, “Loleni ndichoke kuti ndipite ku dziko lakwathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atamva Hadadi ku Ejipito kuti Davide anagona ndi makolo ake, ndi kuti Yowabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atamva Hadadi ku Aigupto kuti Davide anagona ndi makolo ace, ndi kuti Yoabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.