1 Kings 11:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Farao adati, “Chakusoŵa nchiyani kwathu kuno kuti uziti ukufuna kupita ku dziko lakwanu?” Hadadi adauza Farao kuti, “Iyai sizimenezo, mungondilola basi kuti ndizipita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono Farao anati kwa iye, Koma chikusowa iwe nchiyani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?” Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono Farao anati kwa iye, Koma cikusowa iwe nciani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.