1 Kings 11:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu ameneyu adasonkhanitsa anthu, nakhala mtsogoleri wao wa gulu la achifwamba. Izi zidachitika pamene Davide adati atagonjetsa Hadadezere, adapha ankhondo a ku Zoba. Tsono Rezoni ndi gulu lake adapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko, ndipo anthuwo adamlonga ufumu womalamulira dziko la Siriya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, nakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, hakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.