1 Kings 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Rezoni anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, namamvuta Solomoniyo monga momwe Hadadi ankachitira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anali mdani wa Israyeli masiku onse a Solomo, kuonjezerapo coipa anacicita Hadadi, naipidwa nao Aisrayeli, nakhala mfumu ya ku Aramu.