1 Kings 11:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Winanso woukira Solomoni anali Yerobowamu, mwana wa Nebati wa fuko la Efuremu, wa ku Zereda. Anali mmodzi mwa nduna za Solomoni, amene mai wake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yerobowamu mwana wa Nebati Mwefuremu wa ku Zereda mnyamata wa Solomoni, dzina la amake ndiye Zeruya, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lake pa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yerobiamu mwana wa Nebati M-efrati wa ku Zereda mnyamata wa Solomo, dzina la amace ndiye Zeruwa, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lace pa mfumu.