1 Kings 11:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhani ya kuukira kwakeyo idaayenda motere: Solomoni adaamanga linga la Milo, nakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chifukwa chakukweza iye dzanja lake pa mfumu ndi chimenechi: Solomoni anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cifukwa cakukweza iye dzanja lace pa mfumu ndi cimeneci: Solomo anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wace.