1 Kings 11:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yerobowamu anali munthu wolimba mtima, ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo ngwachangu, adamuika kuti akhale kapitao woyang'anira ntchito yathangata m'dziko la ana a Yosefe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang'anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu ameneyo Yerobiamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomo anamuona mnyamatayo kuti ngwacangu, anamuika akhale woyang'anira wa nchito yonse ya nyumba ya Yosefe.