1 Kings 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye tsiku lina pamene Yerobowamu anali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, mneneri Ahiya wa ku Silo adampeza pa mseu. Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano, ndipo aŵiriwo anali okha kuthengoko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobowamu anatuluka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anavaliratu chovala chatsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobiamu anaturuka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anabvaliratu cobvala catsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo.