1 Kings 11:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni ndidzamsiyira fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye adzakhala nalo fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi cha Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye adzakhala nalo pfuko limodzi, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi ca Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israyeli.