1 Kings 11:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzachita zimenezi chifukwa Solomoniyo wandisiya Ine, wayamba kupembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Choncho sadandimvere, sadachite zimene ine ndifuna, ndipo sadasunge malamulo anga ndi malangizo anga, monga momwe ankachitira Davide, bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Azidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amoabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kucita cimene ciyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wace.