1 Kings 11:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe sindidzamlanda ufumu iyeyo. Adzakhalabe wolamulira masiku onse a moyo wake, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndidamsankha, amene ankasunga malamulo anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lace, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ace onse, cifukwa ca Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, cifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.