1 Kings 11:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe mwana wake ndidzamsiyira fuko limodzi kuti pakhalebe Davide mtumiki wanga azidzakhala ndi nyale nthaŵi zonse pamaso panga ku Yerusalemu, mzinda umene ndausankha kuti azindipembedza kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzamninkha mwana wace pfuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale cikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.