1 Kings 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni atakalamba, akazi akewo adamnyengerera kuti azitsata milungu yachilendo. Choncho sadatsate Chauta, Mulungu wake, ndi mtima umodzi, monga ankachitira Davide bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ace anapambutsa mtima wace atsate milungu yina; ndipo mtima wace sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide atate wace.