1 Kings 11:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Solomoni ankafunitsitsa kupha Yerobowamu. Koma Yerobowamu adachoka nathaŵira ku Ejipito, kwa Sisake mfumu yakumeneko. Adakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Solomoni anafuna kupha Yerobowamu, ndipo Yerobowamu anathawira ku Ejipito kwa Sisake mfumu ya Aejipito, nakhala m'Ejipito kufikira imfa ya Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Solomo anafuna kupha Yerobiamu, ndipo Yerobiamu anathawira ku Aigupto kwa Sisaki mfumu ya Aigupto, nakhala m'Aigupto kufikira imfa ya Solomo.