1 Kings 11:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Solomoni adamanga akachisi pa phiri la kuvuma kwa Yerusalemu, kumangira Kemosi, mulungu wonyansa wa Amowabu, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri lili patsogolo pa Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Salomo anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amoabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri liri patsogolo pa Yerusalemu.