1 Kings 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵayankhe kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anyamata anzake amene anakula nawo limodzi aja anamuyankha kuti, “Anthu amene ananena kwa iwe kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa, koma inu peputsani goli lathu,’ uwawuze kuti ‘Chala changa chakanise nʼchachikulu kupambana chiwuno cha abambo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo acinyamata anzace ananena naye, Dati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, Atate wanu analemeretsa gori lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.