1 Kings 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Chauta anali atazikonzeratu zinthuzo, kuti zichitikedi zimene adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu sinamvere pempho la anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Yehova, kukwaniritsa mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunacokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ace amene Yehova ananenetsa Abiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.