1 Kings 12:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele onse akumpotowo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha mfumuyo kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani ku mahema kwanu! Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraelewo adachoka napita ku nyumba zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kumva zopempha zawo, iwo anayankha mfumu kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide, ndi gawo lanjinso mwa mwana wa Yese? Inu Aisraeli, bwererani ku matenti anu! Ziyangʼanira nyumba yako, Iwe Davide!” Kotero Aisraeli anachoka napita ku nyumba zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu Aisrayeli inu; yang'aniranitu, nyumba yako, Davide. Momwemo Aisrayeli anacoka kumka ku mahema ao.