1 Kings 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu, amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma Aisraele onse adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta, nathaŵira ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehobowamu anafulumira kulowa m'galeta wake kuthawira ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli onse anamugeda ndi miyala mpaka kumupha. Koma Mfumu Rehobowamu anakwera msangamsanga galeta wake nathawira ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.