1 Kings 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, adakali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, Yerobowamu adabwerera kuchokera ku Ejipitoko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali m'Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeroboamu mwana wa Nebati anamva zimenezi. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamuyo akukhala ku Igupto, pakuti atathawa Mfumu Solomoni iyeyo anakakhala ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali kuti Yerobiamu mwana wa Nebati anacimva akali m'Aigupto, kumene anathawira kucokera ku maso a Solomo mfumu, pakuti Yerobiamu anakhala ku Aigupto.