1 Kings 12:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono a ku Israele onse atamva kuti Yerobowamu wabwerera kuchokera ku Ejipito, adatumiza mau okamuitana kuti afike ku msonkhano. Kumeneko adamlonga ufumu wolamulira a ku Israele onse. Padaalibe wa ku Israele ndi mmodzi yemwe amene ankatsata ulamuliro wa banja la Davide, kupatula fuko la Yuda lokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse atamva kuti Yeroboamu wabwerera kuchokera ku Igupto, anatumiza mawu okamuyitana kuti abwere ku msonkhano ndipo anamuyika kukhala mfumu ya Aisraeli onse. Fuko la Yuda lokha ndi lomwe linkatsatira nyumba ya Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.