1 Kings 12:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo 180,000 a fuko la Yuda ndi la Benjamini ndi cholinga chakuti akamenyane ndi mafuko a ku Israele, kuti choncho amubwezere Rehobowamu ufumu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rehobowamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi fuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israele, kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini, nasankha ankhondo okwanira 180,000, kuti akamenyane ndi nyumba ya Israeli kuti amubwezere Rehobowamu mwana wa Solomoni ufumu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.