1 Kings 12:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ine Chauta ndikuti musapite kukamenyana ndi abale anu a ku Israele. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nabwerera kwao monga momwe Chauta adaŵalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu Aisraeli. Aliyense wa inu abwerere kwawo, pakuti zimenezi ndachita ndine.’ ” Choncho anthuwo anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera kwawo, monga analamulira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.