1 Kings 12:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ameneŵa akamapita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, mitima yao idzabwerera kwa mbuyao Rehobowamu, mfumu ya ku Yuda, ndipo adzandipha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati anthuwa azipitabe kukapereka nsembe ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, adzayambanso kutsatira mbuye wawo Rehobowamu, mfumu ya Yuda. Adzandipha ndi kubwerera kwa Mfumu Rehobowamu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.