1 Kings 12:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mfumuyo itaganizaganiza pa zimenezi, idapanga mafano aŵiri a anaang'ombe agolide. Tsono idauza anthu kuti, “Inu anthu a ku Israele, ku Yerusalemu mwakhala mukupitako nthaŵi yaitali. Tsopano milungu yanu ndi iyi imene idakutulutsani ku dziko la Ejipito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Itapempha nzeru, mfumuyo inapanga mafano awiri a ana angʼombe. Mfumuyo inati kwa anthuwo, “Mwakhala mukupita ku Yerusalemu nthawi yayitali. Iwe Israeli, nayi milungu yako imene inakutulutsa mʼdziko la Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.