1 Kings 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipepukitsireko goli lolemetsayo ndi ntchito zoŵaŵazo zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri, koma inu chepetsani ntchito yowawa pa ife ndipo peputsani goli lolemetsa limene anatisenzetsa. Mukatero tidzakutumikirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atate wa nu analemeretsa gori lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko nchito zosautsa za atate wanu, ndi gori lolemera lace limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.