1 Kings 12:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani, kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mfumu Rehobowamu anapempha nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira Solomoni abambo ake pamene anali ndi moyo. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu amenewa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Rehabiamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace, akali moyoiyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?