1 Kings 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Madodawo adamuuza kuti, “Mukamatumikira bwino anthu ameneŵa nkukhaladi mtumiki wao, muzilankhula nawo mau abwino, ndipo iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala chikhalire atumiki anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha kuti, “Ngati lero mudzakhala mtumiki wa anthu amenewa ndi kuwatumikira ndipo mukawayankha bwino, iwowo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala cikhalire atumiki anu.