1 Kings 12:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati kwa iwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenza ife?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ngotani? Kodi ndiwayankhe chiyani anthu amene akunena kwa ine kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anatisenzetsa’?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati kwa lwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze gori limene atate wanu anatisenza ife?