1 Kings 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mneneri wa Mulungu adachokera ku Yuda napita ku Betele monga momwe Chauta adaamlamulira. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, munthu wa Mulungu anacokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Beteli; ndipo Yerobiamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.