1 Kings 13:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ku Betele kunkakhala mneneri wina wokalamba. Ana ake adadza kudzamuuza zonse zimene mneneri wa Mulungu adaachita ku Betele tsiku lija. Adauzanso atate ao mau onse amene mneneri wa Mulungu uja adaauza mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ku Betele kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ku Beteli kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wace wina anadzamfotokozera macitidwe onse anawacita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Beteli ndi mau ace anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.