1 Kings 13:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo bambo wao uja adaŵafunsa kuti, “Kodi adadzera njira iti?” Ana akewo adamlangiza njira imene adadzera mneneri wa Mulungu wochokera ku Yuda uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abambo awo aja anawafunsa kuti, “Kodi wadzera njira iti?” Ana akewo anamufotokozera njira imene munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo anadzera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? popeza ana ace adaona njira analowera munthu wa Mulungu anacokera ku Yudayo.