1 Kings 13:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Idalondola mneneri wa Mulungu uja, nikampeza atakhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu. Tsono idamufunsa kuti, “Kodi inu ndiye mneneri wa Mulungu amene mudachoka ku Yuda?” Munthu uja adayankha kuti, “Ndine amene.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anachokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo inalondola munthu wa Mulunguyo. Inamupeza atakhala pansi pa mtengo wa thundu ndipo inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene anabwera kuchokera ku Yuda?” Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndineyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali, tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anacokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.