1 Kings 13:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhalambayo idamuuza kuti, “Inenso ndine mneneri monga inu nomwe, ndipo mngelo adalankhula nane nandiwuza kuti, ‘Ubwerere naye limodzi kunyumba kwako, kuti akadye chakudya ndiponso akamweko madzi.’ ” Nkhalambayo inkamuuza zabodza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneri wokalambayo anayankha kuti, “Inenso ndine mneneri ngati iwe. Ndipo mngelo wa Yehova anayankhula nane mawu a Yehova kuti, ‘Kamubweze abwere ku nyumba yako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’ ” Koma anamunamiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.