1 Kings 13:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mneneriyo adatemberera guwalo potsata mau a Chauta nati, “Guwa iwe, guwa iwe, imva mau a Chauta, akunena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa pa banja la Davide, dzina lake Yosiya. Pa iwe iyeyo adzaperekapo ngati nsembe ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene amafukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lace ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.