1 Kings 13:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo iyeyo adafuulira mneneri wa Mulungu, wochokera ku Yuda uja kuti, “Imvani mau a Chauta, akuti chifukwa choti simudamvere mau a Chauta, ndipo simudatsate lamulo lake limene adakulamulani,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anafuwulira munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo kuti, “Yehova akuti, ‘Iwe wanyoza mawu a Yehova ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napfuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anacokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova, Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,