1 Kings 13:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo popita, adakumana ndi mkango pa mseu, ndipo udamupha. Tsono mtembo udagwera mu mseu, ndipo bulu uja adaima pambali pa mtembowo. Mkango uja nawonso udaima pambali pa mtembowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m'njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akupita, anakumana ndi mkango pa msewu ndipo unamupha, mtembo wake unagwera pansi pa msewu, bulu uja anayima pambali pake ndipo mkango unayima pafupi ndi mtembowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atacoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha, ndipo mtembo wace unagwera m'njiramo, buru naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.