1 Kings 13:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mneneri amene adaabweza mnzake kunjira uja, atamva zimenezo, adati, “Ameneyo ndi mneneri wa Mulungu uja amene sadamvere mau a Chauta. Nchifukwa chake Chauta wampereka kwa mkango, umene wamkadzula ndi kumupha, monga momwe Chauta adaanenera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneri amene anamubweza mnzake ku njira uja atamva zimenezi, anati, “Ameneyo ndi munthu wa Mulungu amene wanyoza mawu a Yehova. Yehova wamupereka kwa mkango umene wamukhadzula ndi kumupha, monga momwe Yehova anamuchenjezera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvera mau a Yehova; cifukwa cace Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.