1 Kings 13:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapita, nakapeza mtembo wa munthu uja uli gone pa mseu, bulu ataima pambali pake pamodzi ndi mkango womwe. Mkangowo sudadye mtembowo kapena kukadzula bulu uja ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapita, nakapezadi mtembo utagwera pansi mu msewu, bulu pamodzi ndi mkango atayima pambali pake. Koma mkangowo sunadye mtembowo kapena kukhadzula buluyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka iye, napeza mtembo wace wogwera m'njira, ndi buru ndi mkango ziti ciimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula buru.