1 Kings 13:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mneneri wokalambayo adatenga mtembo wa mneneri wa Mulungu uja, nauika pa buluyo, ndipo adabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuika mtembowo m'manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mneneri ananyamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa bulu, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mneneri wokalambayo anatenga mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nawuyika pa bulu, ndipo anabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuyika mtembowo mʼmanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mneneri ananvamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa buru, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.