1 Kings 13:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaika mtembowo m'manda ake. Pomulira ankati, “Mbale wanga ine! Mbale wanga ine!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mtembo wake anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anayika mtembowo mʼmanda amene mneneri wokalamba uja anadzikonzera, ndipo anamulira pomanena kuti, “Mʼbale wanga ine! Mʼbale wanga ine!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mtembo wace anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!