1 Kings 13:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo atamuika m'manda adauza ana ake kuti, “Ine ndikafa mudzandiike m'manda m'mene mneneri wa Mulunguyu waikidwa. Mudzaike mtembo wanga pambali pa mtembo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, atamuika iye, ananena ndi ana ake, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atamuyika mʼmanda, iye anati kwa ana ake, “Ine ndikafa, mudzandiyike mʼmanda amene munthu wa Mulungu wayikidwa. Mudzayike mafupa anga pambali pa mafupa ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, atamuika iye, ananena ndi ana ace, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ace.