1 Kings 13:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale zidaatero, Yerobowamu sadasiye njira zake zoipa, koma adaikanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo akeake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna, adampatula kuti akhale wansembe wa pa malowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere pa njira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale izi zinachitika, Yeroboamu sanasiye njira zake zoyipa, koma anasankhanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo ake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna kukhala wansembe iye anamupatula kukhala wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambuyo pa ici Yerobiamu sanabwerera pa njira yace yoipa, koma analonganso anthu acabe akhale ansembe a misanje, yensewakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje,