1 Kings 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Yerobowamu atamva zimene ankanena mneneri wa Mulungu zija za guwa la ku Betele, adatambalitsa dzanja lake ali kuguwako nati, “Mgwireni.” Pomwepo dzanja lake lomwe adaatambalitsira mneneri wa Mulungu lija lidauma kuti gwa, ndipo sadathenso kulibweza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe m'Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, pa kumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawapfuula, kutemberera guwa la nsembe m'Beteli, Yerobiamu anatansa dzanja lace ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lace analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulipfunyatitsanso.