1 Kings 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo guwa lija nalonso lidang'ambika, ndipo phulusa lapaguwapo lidamwazika potsata chizindikiro chimene adaapereka mneneri wa Mulunguyo, malinga ndi m'mene adaanenera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yomweyo guwa lija linangʼambika pakati ndipo phulusa lake linamwazika molingana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapereka potsata mawu a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa cizindikilo cimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Mulungu.