1 Kings 13:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu idauza mneneri wa Mulungu uja kuti, “Mupemphere kwa Chauta Mulungu wanu kuti andikomere mtima, dzanja langali lichire.” Mneneri wa Mulungu adapemphera kwa Chauta, ndipo dzanja la mfumu lidachiradi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Undipempherere kwa Yehova Mulungu wako kuti andikomere mtima ndipo undipempherere kuti dzanja langa lichire.” Choncho munthu wa Mulungu anapempha kwa Yehova, ndipo dzanja la mfumu linachiritsidwa nʼkukhala ngati momwe linalili kale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika