1 Kings 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidzagwetsa mavuto pa banja lako, iwe Yerobowamu. Ndidzaononga mwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yomwe, m'dziko la Israele. Ndidzaononga kwathunthu banja la Yerobowamu monga m'mene munthu amachotsera ndoŵe pa bwalo mpaka yonse itatha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka m'Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, taona, ndidzafikitsa coipa pa nyumba ya Yerobiamu, ndi kugurula mwana wamwamuna yense wa Yerobiamu womangika ndi womasuka m'Israyeli, ndipo ndidzacotsa psiti nyumba yonse ya Yerobiamu, monga munthu acotsa ndowe kufikira idatha yonse.