1 Kings 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense m'banja la Yerobowamu, amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zidzamudya. Ndatero Ine Chauta.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Agalu adzadya aliyense wa Yerobowamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Agaru adzadya ali yense wa Yerobiamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.